Micah 3

Atsogoleri ndi Aneneri Adzudzulidwa

1Ndipo ine ndinati,

“Tamverani, inu atsogoleri a Yakobo,
inu olamulira nyumba ya Israeli.
Kodi sindinu oyenera kudziwa kuweruza molungama,
2inu amene mumadana ndi zabwino ndi kukonda zoyipa;
inu amene mumasenda khungu la anthu anga,
ndipo mumakungunula mnofu pa mafupa awo;
3inu amene mumadya anthu anga,
mumasenda khungu lawo
ndi kuphwanya mafupa awo;
inu amene mumawadula nthulinthuli
ngati nyama yokaphika?”

4Pamenepo adzalira kwa Yehova,
koma Iye sadzawayankha.
Nthawi imeneyo Iye adzawabisira nkhope yake
chifukwa cha zoyipa zimene anazichita.
5Yehova akuti,

“Aneneri amene
amasocheretsa anthu anga,
ngati munthu wina awapatsa chakudya
amamufunira ‘mtendere;’
ngati munthu wina sawapatsa zakudya
amamulosera zoyipa.
6Nʼchifukwa chake kudzakuderani,
simudzaonanso masomphenya,
mdima udzakugwerani ndipo simudzawombezanso.
Dzuwa lidzawalowera aneneriwo, ndipo mdima udzawagwera.
7Alosi adzachita manyazi
ndipo owombeza mawula adzanyazitsidwa.
Onse adzaphimba nkhope zawo
chifukwa Mulungu sakuwayankha.”

8Koma kunena za ine, ndadzazidwa ndi mphamvu,
ndi Mzimu wa Yehova,
ndi kulungama, ndi kulimba mtima,
kuti ndilalikire za kugalukira kwa Yakobo,
kwa Israeli za tchimo lake.
9Imvani izi, inu atsogoleri a nyumba ya Yakobo,
inu olamulira nyumba ya Israeli,
inu amene mumadana ndi kuweruza kolungama;
ndipo mumakhotetsa zinthu zonse zolondola;
10inu amene mukumanga Ziyoni pokhetsa magazi,
ndi Yerusalemu ndi kuyipa kwanu.
11Atsogoleri ake amalandira chiphuphu kuti aweruze,
ansembe ake amalandira malipiro kuti alalikire,
ndipo aneneri ake amanenera kuti alandire ndalama.
Komatu amatsamira pa Yehova nʼkumanena kuti,
“Kodi Yehova sali pakati pathu?
Palibe tsoka limene lidzatigwere.”
12Choncho chifukwa cha inu,
Ziyoni adzatipulidwa ngati munda,
Yerusalemu adzasanduka bwinja,
ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango yowirira.
Copyright information for NyaCCL